/
KUYAMBA ULENDO MU CHIKHULUPIRIRO KUYAMBA ULENDO MU CHIKHULUPIRIRO

KUYAMBA ULENDO MU CHIKHULUPIRIRO - PowerPoint Presentation

finestlaxr
finestlaxr . @finestlaxr
Follow
352 views
Uploaded On 2020-10-06

KUYAMBA ULENDO MU CHIKHULUPIRIRO - PPT Presentation

Phunziro 13 September 26 2020 Kukhazikitsa njira Yesu Chiyambi cha ulendo Petro Yohane Mateyu Kufikira Cholinga Paulo Kuyambiranso ulendo ID: 813187

ndi yesu cha kuti yesu ndi kuti cha chikondi moyo petro wake chake kwa koma chifukwa mulungu yohane ife

Share:

Link:

Embed:

Download Presentation from below link

Download The PPT/PDF document "KUYAMBA ULENDO MU CHIKHULUPIRIRO" is the property of its rightful owner. Permission is granted to download and print the materials on this web site for personal, non-commercial use only, and to display it on your personal computer provided you do not modify the materials and that you retain all copyright notices contained in the materials. By downloading content from our website, you accept the terms of this agreement.


Presentation Transcript

Slide1

KUYAMBA ULENDO MUCHIKHULUPIRIRO

Phunziro

13,

September

26, 2020

Slide2

Kukhazikitsa

njira

:

Yesu

Chiyambi cha ulendo: Petro, Yohane, MateyuKufikira Cholinga: PauloKuyambiranso ulendo: Kodi mukonda ine?Njira ya Chikondi: Chimwemwe pa kugawana

Kuyamba kuyenda muchikhulupiriro ndikofunikira kuti tipeze Chimwemwe potenga nawo mbali mu utumiki wo itanira abwenzi kwa Yesu.Yesu anationetsa ife njira kudzera mu chitsanzo chake. Iyi ndi njira yomwe ena anatenga kale.Chimwemwe sichinasungidwe kwa mphotho yomaliridzira yokha, koma chili mbali yaulendo. Timadzadzidwa ndi Chimwemwe tikaona ena akulandira Yesu kukhala mpulumutsi wa moyo wawo.

Slide3

KUKHAZIKITSA NJIRA“

Mukhale

nao

mtima m'kati mwanu umene unalinso mwa Khristu Yesu.” (Afilipi 2:5)

Yesu ndi Mulungu, koma anasankha “kusiya” kaye ulemerero wake pamene anasiya mpando wake kumwamba monga mfumu yadziko ndikudzakhala munthu (Afilipi. 2:6-7).Sanababwe ngati munthu otchuka, koma ngati kapolo odzichepetsa. Kuphatikiza pamenepa: Anagonjera kwathunthu chifuniro cha Mulungu, nakhala omvera kufikira imfa ya pa mtanda chifukwa cha chikondi chake

pa ife. (Afilipi. 2:8).

Chifukwa

cha

chikondi

chopanda

undekha ichi, Mulungu “anamukweza, namupatsa dzina limene

liposa maina onse.” (Afilipi. 2:9). Komabe, Chisangalalo chake

chachikulu sichinali kukwezedwako,

koma kuti “Adzaona zotsatira za mavuto a moyo wake nadzakhutitsidwa

nazo.” (Yesaya. 53:11)Pamene tikutsata mayendedwe a

chikhulupiriro a Yesu, Chisangalalo

chathu chachikulu chidzakhala kuona anthu akupereka miyoyo

yawo

kwa

mpulumutsi

,

ndikudzakhala

moyo wamuyaya ndi Yesu.

Slide4

CHIYAMBI CHA ULENDO

Ndipo

iwo

anasiya pomwepo makokawo, namtsata Iye.” (Mateyu 4:20)Andrea, Petro, Yohane, ndi Yakobo anali atamutsata Yesu kwa kanthawi. Pambuyo

pake, anaitanidwa kuti amutsate “nthawi zonse.” Yesu anawalimbikitsa kuti asiye kukhala asodzi a nsomba nakhala “asodzi a anthu.” (Mateyu. 4:19).Anasiya chirichonse nadzipereka kugawana ndi ena za chikondi cha Yesu.Mateyu analinso munthu wina amene Yesu anamuitana kuti

aleka zina zonse. Yesu anadziwa zokhumba za mtima wake, anamulimbikitsa kusinthitsa moyo

wake ofewa koma osakhutitsidwa ndi moyo

okhala ndi cholinga

ndikukhutitsidwa (Matthew 9:9).

Ifenso, tikufuna kukhala moyo wopindula china chake,

wopambana ndi wokhala nacho

cholinga chabwino, chotero tiyankhe kuitana kwa

Khristu kuti timutsate.

Slide5

KUFIKIRA CHOLINGA

Ndalimbana

nako

kulimbana kwabwino, ndatsiriza njirayo, ndasunga chikhulupiriro.” (2 Timoteo 4:7)Ndani angasankhe mdani wawo woipitsitsa kukhala mneneri wawo?

Saulo (Paulo) ndi chitsanzo cha munthu amene sitingamusankhe kukhala olalikira uthenga wabwino, koma Yesu anamusankha. Zingatheke bwanji kuti anthu osayembekezereka nkukhala alaliki akulu (Mwamuna ogwidwa ziwanda, Mzimayi wa ku Samariya, hule, otolera misonkho, “osaphunzira” asodzi, opha akhristu…)?Chisomo cha mulungu chinasintha mitima yawo

. Ndipo anadzipereka kukauza ena za zozizwa zomwe Mulungu anachita miyoyo

yawo.

Paulo

sanasiye

kutsatira

cholinga

chake

kuyambira

pomwe anakomana ndi Yesu. Anapereka MOYO WAKE WONSE kulalikira

uthenga

wabwino

.

Slide6

KUYAMBIRANSO ULENDO

Ananena

naye

kachitatu, ‘Simoni, mwana wa Yona, kodi undikonda ine?’ Petro anamva chisoni kuti anati kwa

iye kachitatu, ‘Kodi undikonda Ine?’ Ndipo anati kwa iye, ‘Ambuye, mudziwa inu zonse; muzindikira kuti ndikukondani inu

.’ Yesu ananena naye

, ‘Dyetsa

nkhosa

zanga.’” (

Yohane 21:17)

Petro anachita tchimo lalikulu

: Anamukana Yesu(Marko. 14:66-72). Anazimva kuti sangathe

kupitiriza kuudza ena za Yesu.

Koma

,

Yesu

anadziwa

mtima

wa

Petro,

Anadziwa

kuti

Petro

amamukondabe

. Nchifukwa chake

anamufunsa pagulu kuti avomereze za chikondi chake pa Iye

katatu

.

Yesu

anabwezeretsa

kudzidalira

kwa

Petro

ndi

kumupatsa

utumiki

:

Kuyangánira

mpingo wake

ndi

kulalikira

uthenga

wabwino

.

Kumene

kuli

kuonetsa chikondi chake mu ntchito

Mwina

mwamukanako

Yesu

kudzera

mu

ntchito

zanu

koposa

kamodzi

.

Nkhani

yabwino

ndiyakuti

chisomo

chikupezekabe

,

ndipo

mukungu

sanathane

nanu

. Malo

akadalipo

mu

ntchito

yake

ngati

muli

olola

.

Slide7

NJIRA YA CHIKONDI

Umo

tizindikira

chikondi, popeza Iyeyu anapereka moyo wake chifukwa cha ife; ndipo ife tiyenera

kupereka moyo wathu chifukwa cha abale.” (1 Yohane 3:16)Yesu anamubwezeretsa Petro ndikulola kuti akhale nacho chisangalalo chachikulu mmoyo uno: Kuona miyoyo ikulowa mu ufumu wa Mulungu.Petro anaona zipatso zoyamba kuchokera mu

ulaliki wake pa tsiku la Pentecost (Machitidwe 2:14-41). Petro anasonyeza chikondi chomwe anachivomereza pa maso a Yesu

ndi ophunzira ake.

Petro

anayenera

kulipira

chikondi ndi chisangalalo chimenechi, mapeto ake

anataya moyo wake (Yohane 21:18-19).

Pambuyo pake Yohane analongosola kuti chikondi

chimaphatikizanso kuzipereka, nsembe yosazikonda, yosayembekezera mphoto

ina iriyonse.

Tsiku lomwe tidzakhale ndi Yesu ndi

opulumutsidwa

(

kuphatikiza

omwe

anamudziwa

Yesu chifukwa cha ife),

sitidzaonanso kanthu kamene tinachita pa dziko lino monga nsembe. Kutsatira Yesu

mpaka kumapeto kudzakhala

kokwanira

Slide8

“Mzimu Woyera atatsika, pamene

ophunzira

anapita

kukalalika za mpulumutsi wa moyo, chokhumba chawo chachikulu chinali chipulumutso cha miyoyo. Anakondwera posonkhana ndi opulumutsidwa. Anali

okoma mtima, oganiza bwino, odziletsa,okonzeka kudzipereka chifukwa cha choonadi. Mukukhala kwawo tsiku ndi tsiku anaonetsera chikondi chomwe Khristu anachionetsa kwaiwo. Posanena kapena kuchita

modzikonda anayatsa chikondi mitima

ya ena”

E.G.W. (The Acts of the Apostles, cp. 54, p. 547)

Related Contents


Next Show more