Patangotsala pangono kuti Petro amukane Yesu anamuuza Petro kuti Ndipo iwe pamene watembenuka ukhazikitse abale ako Luka 2232 Petro adakwaniritsa ID: 785753
Download The PPT/PDF document "UTUMIKI WA PETRO Phunziro 6 la pa Aug..." is the property of its rightful owner. Permission is granted to download and print the materials on this web site for personal, non-commercial use only, and to display it on your personal computer provided you do not modify the materials and that you retain all copyright notices contained in the materials. By downloading content from our website, you accept the terms of this agreement.
Slide1
UTUMIKI WA PETRO
Phunziro 6 la pa August 11, 2018
Slide2Patangotsala pang’ono kuti Petro amukane, Yesu anamuuza Petro kuti “Ndipo iwe, pamene watembenuka ukhazikitse abale ako” Luka 22:32.Petro adakwaniritsa langizoli pozungulira ndi kularikira uthenga wabwino
malo
osiyanasiyana, kutumikira abale ake , anthu osowa, okaikakaika, komanso alendo okhalanawo mdziko.
Utumiki wa Petro.Utumiki wa machiritso. Machitidwe 9:32-43.Utumiki kwa amitundu. Machitidwe 10:1-43.Utumiki wa kuvomereza amitundu.Machitidwe 10:44-11:1-18.Utumiki wa mpingo.Kulalikira kwa amitundu. Machitidwe 11:19-30.Chisautso ndi kulondedwalondedwa kwa Ekelesia. Machitidwe 12.
Uthenga
udalalikidwanso kwa anthu amitundu okhala ku Antiyokeya.
Slide3Machitidwe 9:32-43UTUMIKI WA MACHIRITSO
“
Ndipo Petro anagwira
dzanja lache , namnyamutsa ; ndipo m’mene adaitana oyera mtima ndi amasiye , anampereka iye wamoyo” (Machitidwe 9:41)Mulungu adagwiritsa ntchito Petro kuchita zozizwa zofanana
ndi zomwe Yesu Kristu adazichita.
Luka 5:17-26
“
Ndinena
kwa
iwe
,
Tauka
,
nusenze
kama wako numuke kunyumba kwako."
Machitidwe 9:32-35
“Eneya Yesu Kristu akuchilitsa iwe. Uka yalura mphasa yako”
Marko 5:35-43
“Komai Iye anawatulutsa onse ……… “ Buthu, ndinena ndi iwe, uka”
Machitidwe 9:36-43
“
Koma
Petro
anawaturutsa
onse
…………… “ Tabita,
uka
”
Slide4Machitidwe 9:32-43Zotsatira za machiritso onsewa zinalizofanana; “ ambiri analemekeza Mulungu”, “ anthu anatembenukira kwa Ambuye” “ ambiri anakhulupilira
Ambuye” ndinso “ ambiri anagwidwa ndi kuzizwa kwakukulu”.
UTUMIKI WA MACHIRITSO“Ndipo Petro
anagwira dzanja lache
, namnyamutsa ; ndipo m’mene adaitana oyera
mtima
ndi
amasiye
,
anampereka
iye wamoyo” (
Machitidwe 9:41)
Pamene
talolera mwaphumphu kuti Mulungu Yehova atigwiritse ntchito mu utumiki wa uthenga wabwino,zazikulu zitha kuchitika.
Slide5Ngero wa Yehova anamuuza Korneliyo amene ayenera
kumuitana
ndi kumalo kumene
munthuyo akupezeka.Kutengere pa kamvetsetsedwe ka nkhani ya chipulumutso pakati pa a Yuda, Petro monga muyuda weneweni otsata chilamulo, sadafuna kulowa
mnyumba ya munthu wa
amitundu.Chfukwa cha ichi
Mulungu
adagwiritsa
ntchito
masomphenya
apadera kumuuza Petro kuti
akalalikire uthenga wabwino
kwa amitundu.
Machitidwe 10:1-43UTUMIKI KWA AMITUNDU“Ndipo Petro anatsegula pakamwa pache
, nati
; Zoonadi ndizindikira kuti Mulungu alibe tsankhu.” (Machitidwe 10:34)
Yesu
Khristu adagwiritsa ntchito chitsanzo cha Petro kutiphunzitsa kuti chipulumutsa ndi cha aliyense
posayan’ganira mtundu
ndi
manenedwe
(Tito 2:11,
Agalatiya
3:26-28,
Aefeso
2:11-19).
Palibe
tsankho
,
chisomo
cha
Mulungu
chaperekedwa
kwa
onse
.
Kotero
tikuyenera
tilalikire
uthenga
wabwino
kwa
aliyense
.
Slide6Machitidwe 10:44-11:1-18UTUMIKI WAKUVOMELEZA ACHIKUNJA“Ndipo pamene
anamva izi, anakhala du,
nalemekeza Mulungu, ndi kunene, Potero Mulungu anapatsa kwa amitundinso kutembenukira mtima ku moyo” (Machitidwe 11:18)Petro anaona amitundu akulandira Mzimu Oyera “ Monga anatero ife poyamba paja” Kotero anamvetsetsa
kuti amitunduwa atha kubatizidwa ndikukhala mbali
imodzi ya ziwalo za mpingo popanda m’dulidwe.Koma mpingo wa nthawi imeneyo sunali
okonzeka
kuwavomeleza
amitunduwa
kuti akhale mbali imodza ya ziwalo
za mpingo.Adatsutsana ndi chimene Petro adachita potengera uthenga kwa amitundu
. Koma pamene Petro adafotokoza nthano yonse ya momwe zidachitikira anthuwo adagonjera navomereza.
Khomo lidatseguka kwa amitundu. Ichi
chinabweretsa zotsatila zazikulu patsogolo pake.
Slide7Machitidwe 11:19-30KULALIKIRA KWA AMITUNDU
“
Koma panali ena
mwa iwo, amuna a ku Kupro, ndi Kurene, amenewo, m’mene dafika ku Antiokeya, analamkhula ndi a Helene, ndikulalikila uthenga wabwino
wa Ambuye Yesu
Khristu”. (Machitidwe 11:20)Okhulupilira
ambiri
anathawa
ku
Yerusalem
chifukwa cha chisautso chachikulu
chotsogozedwa ndi Saulo. Adalalikira uthenga wabwino kwa muyuda aliyense adakomana naye. Ena
mwa iwo adaganiza zokalalikira uthenga kwa amitundu ku Antiokeya.Mulungu
adakonzetsera dongosolo lonse. Saulo adasandulika nakhala
mtumwi, Petro adayamba kulalikira uthenga kwa amitundu ndipo mpingo udawalandira amitunduwo.Pamene mpingo udamva kuti amitundu atembenuka mtima ku Antiokeya , udatumiza Barnaba “Chifukwa anali munthu wabwino, ndi odzala ndi mzimu oyera ndi chikhulupiliro”, amamudziwa Paulo, amadziwanso
kumalo komwe Paulo amapezeka.Barnaba ndi Paulo
analalikira limodzi uthenga wabwino ku Antiokeya kwa chaka chimodzi. Okhulupilira ku Antiokeya anatchedwa ‘ Akhristu” kwa nthawi yoyamba.
Slide8Machitidwe 12KUZUNZIKA NDI KULONDEDWALONDEDWA
“
Koma nyengo
imeneyo Herod mfumu anathira manja ena a m, Ekelesia kuwachitira zoipa. Ndipo anapha ndi lupanga Yakobo mbale wa Yohane
” (Machitidwe 12:1-2)
Mdaniyo ( satana ) adakwiya ndi kukula kwa mpingo, nagwiritsa
ntchito
Herodi
pofuna
kuimitsa ntchito ya uthenga wabwino.
Imfa
ya
Yakobo
ndi kuikidwa mndende kwa Petro kudadandaulitsa mpingo.Herodi adayesetsa kuti Petro asathawe mundende chifukwa atumwi ena amatuluka mndende mosavuta. Machitidwe 5:17-20.Mpingo unakhala pamodzi ndi kupemphera, ndipo Mulungu adamva mapemphero
awo, natuma mngero wache namasula Petro mundende.
Herodi anavulazidwa ndi mngero wa Mulungu kumapeto kwake.
Slide9“Kristu sadayang’ane kusiyana kwa mitundu, udindo ndi manenedwe. Alembi
ndi Afarisi adakhumba kupanga mphatso
yaulere ya kumwamba kukhala yawo yokha monga a Yuda, nasiya kunja ena onse opezeka padziko lapansi. Koma Yesu Khristu anadza kudzaphwasula makoma akugawikana. Anabwera
kudzaonetsa kuti monga mpweya, kuwala
, ndi mvura zitsitsimutsa dziko lapansi
popanda
kusankha
,
mphatso
yache
ya chifundo ndi chikondi yaperekedwa
kwa wina aliyense okhala pa
dziko lapansi. Moyo wa
Yesu Kristu udakhazikitsa chipembedzo chimene sichiona malire a mtundu wina ulionse, chipembedzo chimene ayuda ndi amitundu , mfulu ndi kapolo , ndi olumikizana mu ubale
umodzi , ofanana pamaso
pa Mulungu. Ndondomeko za mayendetsedwe adziko ( policy ) sizinatenge gawo pa mayendetsedwe a ntchito yake ya uthenga wabwino. Sadasiyanitse pakati pa
anansi ndi alendo
, abale ndi adani. Mtima wake nthawi zonse unakhudzika ndi miyoyo yodzala ndi ludzu la madzi amoyo”E.G.W. (The ministry of healing cp. 1,p 25)