/
KUTUMIKIRA MONGA YESU Phunziro KUTUMIKIRA MONGA YESU Phunziro

KUTUMIKIRA MONGA YESU Phunziro - PowerPoint Presentation

reimbursevolkswagon
reimbursevolkswagon . @reimbursevolkswagon
Follow
344 views
Uploaded On 2020-10-06

KUTUMIKIRA MONGA YESU Phunziro - PPT Presentation

8 August 22 2020 Kuunika kwa dziko lapansi Thandizo lokoma mtima Kupereka zosowa zawo Chinthu chofunika kwambiri Zofunikira kwa Yesu Yesu anachita ID: 813186

yesu kwa kuti ndi kwa yesu ndi kuti lapansi dziko ena iye mwa omwe kuunika moyo ndipo anali anthu

Share:

Link:

Embed:

Download Presentation from below link

Download The PPT/PDF document "KUTUMIKIRA MONGA YESU Phunziro" is the property of its rightful owner. Permission is granted to download and print the materials on this web site for personal, non-commercial use only, and to display it on your personal computer provided you do not modify the materials and that you retain all copyright notices contained in the materials. By downloading content from our website, you accept the terms of this agreement.


Presentation Transcript

Slide1

KUTUMIKIRA MONGA YESU

Phunziro

8,

August

22, 2020

Slide2

Kuunika kwa dziko lapansiThandizo lokoma mtimaKupereka zosowa

zawoChinthu chofunika kwambiriZofunikira kwa Yesu

Yesu anachita zambiri

pambali pa kulalikira za ufumu wa kumwamba

. Ankakhala pamodzi ndi anthu, kumvetsera

zonena zawo, komanso kuwachitira zabwino

.Yesu anawathandiza m’mavuto pnse amene anadza nawo kwa

iye.Iye ali chitsanzo

chathu

pamene tikutumikira.

Slide3

KUUNIKA KWA DZIKO LAPANSI

“Pamenepo Yesu

analankhulanso nao

, nanena,

Ine

ndine kuunika

kwa dziko

lapansi;

iye

wonditsata

Ine sadzayenda

mumdima, koma adzakhala

nako

kuunika

kwa moyo

.’”

(

Yohane

8:12)

Yesu anabwera pa dziko lapansi kudzachotsa mdima wa uchimo ndi kuunika kwa chipulumutso (Yohane 1:4-5; 3:19-21).

Khalani Mchere. Mchere ukuyenera kusakanizika ndi chakudya kuti ulowerere ndi kukometsa chakudyacho. Tikuyenera tikhala mu dziko lapansi kuti uthenga wabwino ulowere bwino (Yohane 17:15-18).Khalani Kuunika. Kuwala kupezeka mumdima omwe ukupezeka ku malo omwe timakhala, mmidzi, ndi mmizinda, kuwaunika ndi kuwala kwa ulemerero wa mulungu (Afilipi 2:15).

Anakhala pakati pa anthu kuti akwaniritse izi. “Anali kuchitira anthu za bwino ndi kuchiritsa onse” (Machitidwe 10:38).

Anatilimbitsa

ife

kumutsatira

kupyolera

mu

zitsanzo

ziwiri

izi

(

Mateyu

5:13-14):

Slide4

“Sicholinga cha Mulungu kuti tidzipatule

ku dziko lapansi. Koma kuti

pamene tikadali

mudziko lapansi

tidzipatule tokha kwa

Mulungu. Sitiyenera

kutsatira zochitika za dziko lapansi

. Tikuyenera kukhala

mudziko

lapansi

monga zokometsera, monga mmene

mchere umasunga kukoma kwake.

Pakati pa anthu

ochimwa, odetsedwa,

opembedza mafano, tiyenera

kukhala oyera

,

kusonyeza

kuti mu chisomo cha Khristu

yakubwerezeretsa chiyero mwa munthu. Tikuyenera kuonetsera mphamvu ya kupulumutsa ku dziko lapansi.”E.G.W. (Counsels on Health, p. 592)

Slide5

THANDIZO LOKOMA MTIMA“

Mau anu akhale mçhisomo

, okoleretsera,

kuti mukadziwe

inu mayankhidwe

anu a

kwa yense akatani.

” (Akolose

4:6)

Yesu

anapeze ndi kuonetsera mankhalidwe abwino mwa ena (Mateyu

8:10; Marko 12:34).Chotero, mitima yawo inali yomatseguka kulandira mau a Yesu

.Yesu anali okoma mtima

kwambiri kotero kuti anali kusamalitsa

kuti asadzudzule mokhumudwitsa iwo omwe

anali atangokhulupirira. Yesu anali okoma

mtima

kwambiri kotero amakhutitsa ka chikhulupiriro kakangóno nkati mwa

mitima yawo (Yesaya 42:3).Tiyambe tapeza zinthu zabwino mwa amene atizungulira ndipo tiwaonetse anthu za ubwino wawo

. Mu njira iyi tidzakhudza miyoyo yawo mwapadera.

Slide6

KUPEREKA ZOSOWA ZAWO

” Ndipo onani,

anabwera naye

kwa Iye

munthu wamanjenje

, wakugona pamphasa

: ndipo Yesu pakuona

chikhulupiriro chao,

anati

kwa

wodwalayo, Limba mtima,

mwana, machimo ako akhululukidwa

.(Matthew 9:2)

Yesu anazindikira

zosowa za ena ndipo anabwezeretsa

ku thupi, m’malingaliro, m’maganizo komanso

muuzimu

.

Amathetsa mavuto awo ndikuwaitanira kuti afunefune moyo wa

muyaya : “Machimo ako akhululukidwa”; “Chikhulupiriro chako chakupulumutsa iwe”; “Pita usakachimwenso.” (Mateyu 9:2; Luka 8:48; Yohane 8:11)Tiyenera kukwaniritsa zosowa za ena ndikuyesera kukwaniritsa ngati

tingathe.Pamene tikwaniritsa zosowa zawo, timatsegulanso khomo kuwaonetsera mmene angakwaniritsire chosoweka chachikulu kwa aliyense (ngakhale asakudziwa): Kumasulidwa ku uchimo, moyo osatha; amene ali, Yesu.

Slide7

CHINTHU CHOFUNIKA KWAMBIRI“Ndipo

Yesu anayendayenda m'mizinda

yonse ndi

m'midzi, namaphunzitsa

m'masunagoge

mwao, nalalikira

Uthenga Wabwino wa

Ufumuwo, nachiritsa

nthenda

iliyonse ndi zofooka zonse

.”(

Mateyu 9:35)

Utumiki

wa Yesu

unakhazikika

pa ngodya

zitatu:Kodi ngodya yopambana kwambiri kwa Yesu inali

iti? (Marko 1:38)Iye anabwera pa dziko lapansi “kufunafuna ndi kupulumutsa chotaikacho.” (Luka 19:10). Chotero, kulalikira za chipulumutso ndi kuphunzitsa ena kunali kopambana kwambiri.Pambali pa ichi, kuchiza inali njira yoonetsera khalidwe leni leni la Mulungu komanso kupereka moyo wosatha.

Slide8

ZOFUNIKA KWA YESU

‘Pakuti ndidzakubwezera

iwe

moyo, ndipo

ndidzapoletsa mabala

ako, ati Yehova

,’”

(

Yeremiya

30:17)

Mulungu

anagwiritsa ntchito aneneri kuyankhula za nthenda yosachiritsidwa : Tchimo (Yesaya 1:5;

Yeremiya 30:12).Yesu akufunitsitsa aliyense

achiritsidwe ku nthenda imeneyi, ndikuona

omwe achiritsidwa kale akubweretsa machiritso kwa

ena.

Yesu

anagwiritsa

ntchito mafanizo atatu kunena za masiku otsiriza mu buku la Mateyu 25. Amatilimbikitsa kuti tidzadzidwe ndi Mzimu Woyera and kugwiritsa ntchito mphatso

zomwe zapatsidwa kwa ife mokhulupirika.Mufanizo lomalizira anafotokoza za makhalidwe a akhristu owona. Amene akhala moyo otumikira ena osati odzikonda adzalandiridwa kwa Iye.

Slide9

“Chisomo cha Khristu chomwe

chaululiridwa kwa ife chiyenera kuuluridwa

kwa ena

mwa chikondi.

Chisoni komanso chifundo

chachikulu chizadzadza

miyoyo ya iwo omwe

akadali m’manja

mwa

Satana

. Khristu akuyenera kuchulukitsidwa mwa

amuna ndi akazi onse

omwe amukhulupirira

Iye, chifukwa akuyenera

kukhala mmoyo

wa Khristu pa

kudalitsa

,

kuunikira komanso kubweretsa

chiyembekezo, mtendere ndi Chimwemwe m’mtima ya ena.”E.G.W. (Our Father Cares, May 20)